YOSWA 21
21
Midzi yokhalamo Alevi
1Pamenepo akulu a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazara wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele; 2#Num. 35.2nanena nao ku Silo m'dziko la Kanani, ndi kuti Yehova analamulira mwa dzanja la Mose kuti atipatse midzi yokhalamo ife, ndi mabusa a zoweta zathu. 3Ndipo ana a Israele anapatsa Alevi, kutapa pa cholowa chao, monga mwa lamulo la Yehova, midzi iyi ndi mabusa ao.
4Ndipo maere anatulukira mabanja a Akohati; ndipo molota maere ana a Aroni wansembe, ndiwo Alevi, analandira motapa pa fuko la Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la Benjamini, midzi khumi ndi itatu.
5Ndipo ana otsala a Kohati analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Efuremu, ndi pa fuko la Dani, ndi pa fuko la Manase logawika pakati, midzi khumi.
6Ndipo ana a Geresoni analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Isakara, ndi pa fuko la Asere, ndi pa fuko la Nafutali, ndi pa fuko la Manase logawika pakati m'Basani, midzi khumi ndi itatu.
7Ana a Merari, monga mwa mabanja ao, analandira motapa pa fuko la Rubeni, ndi pa fuko la Gadi, ndi pa fuko la Zebuloni midzi khumi ndi iwiri.
8Motero ana a Israele anapatsa Alevi midzi iyi ndi mabusa ao, molota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose. 9Ndipo anapatsa motapa pa fuko la ana a Yuda, ndi pa fuko la ana a Simeoni, midzi iyi yotchulidwa maina ao; 10kuti ikhale ya ana a Aroni a mabanja a Akohati, a ana a Levi, pakuti maere oyamba adatulukira iwowa. 11#Gen. 23.2Ndipo anawapatsa mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, womwewo ndi Hebroni, ku mapiri a Yuda, ndi mabusa ake ozungulirapo. 12#Yos. 14.14Koma minda ya mudzi ndi milaga yake anapatsa Kalebe mwana wa Yefune, ikhale yake.
13Ndipo kwa ana a Aroni wansembe anapatsa Hebroni ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzake, ndi Libina ndi mabusa ake; 14ndi Yatiri ndi mabusa ake, ndi Esitemowa ndi mabusa ake; 15ndi Holoni ndi mabusa ake, ndi Debiri ndi mabusa ake; 16ndi Aini ndi mabusa ake, ndi Yuta ndi mabusa ake, ndi Betesemesi ndi mabusa ake; midzi isanu ndi inai yotapira mafuko awiri aja. 17Ndipo motapira fuko la Benjamini, Gibiyoni ndi mabusa ake, Geba ndi mabusa ake, 18Anatoti ndi mabusa ake, ndi Alimoni ndi mabusa ake; midzi inai. 19Midzi yonse ya ana a Aroni, ansembe, ndiyo khumi ndi itatu, ndi mabusa ao.
20Ndipo mabanja a ana a Kohati, Aleviwo, otsala a ana a Kohati, analandira midzi ya maere ao motapira pa fuko la Efuremu. 21#Yos. 20.7-8Ndipo anawapatsa Sekemu ndi mabusa ake ku mapiri a Efuremu, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Gezere ndi mabusa ake; 22ndi Kibizaimu ndi mabusa ake, Betehoroni ndi mabusa ake; midzi inai. 23Ndipo motapira fuko la Dani, Eliteke ndi mabusa ake, ndi Gibetoni ndi mabusa ake; 24Ayaloni ndi mabusa ake, Gatirimoni ndi mabusa ake; midzi inai. 25Ndipo motapira pa fuko la Manase logawika pakati, Taanaki ndi mabusa ake, ndi Gatirimoni ndi mabusa ake; midzi iwiri. 26Midzi yonse ya mabanja a ana otsala a Kohati ndiyo khumi ndi mabusa ao.
27 #
Yos. 20.8
Ndipo anapatsa ana a Geresoni, a mabanja a Alevi, motapira pa fuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basani ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo; ndi Beesetera ndi mabusa ake; midzi iwiri. 28Ndipo motapira pa fuko la Isakara, Kisiyoni ndi mabusa ake, Daberati ndi mabusa ake; 29Yaramuti ndi mabusa ake, Enganimu ndi mabusa ake; midzi inai. 30Ndipo motapira pa fuko la Asere, Misala ndi mabusa ake, Abidoni ndi mabusa ake; 31Helekati ndi mabusa ake, ndi Rehobu ndi mabusa ake; midzi inai. 32#Yos. 20.7Ndipo motapira pa fuko la Nafutali, Kedesi m'Galileya ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Hamotidori ndi mabusa ake, ndi Karitani ndi mabusa ake, midzi itatu. 33Midzi yonse ya Ageresoni monga mwa mabanja ao ndiyo midzi khumi ndi itatu ndi mabusa ao.
34Ndipo anapatsa kwa mabanja a ana a Merari, otsala a Alevi, motapira pa fuko la Zebuloni, Yokoneamu ndi mabusa ake, ndi Karita ndi mabusa ake, 35Dimina ndi mabusa ake, Nahalala ndi mabusa ake; midzi inai. 36#Yos. 20.8Ndipo motapira pa fuko la Rubeni, Bezeri ndi mabusa ake, ndi Yahazi ndi mabusa ake, 37Kedemoti ndi mabusa ake, ndi Mefaati ndi mabusa ake; midzi inai. 38#Yos. 20.8Ndipo motapira m'fuko la Gadi, Ramoti m'Giliyadi ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake; 39Hesiboni ndi mabusa ake, Yazere ndi mabusa ake: yonse pamodzi midzi inai. 40Yonseyi ndiyo midzi ya ana a Merari monga mwa mabanja ao, ndiwo otsala a mabanja a Alevi; ndipo gawo lao ndilo midzi khumi ndi iwiri.
41 #
Num. 35.7
Midzi yonse ya Alevi, pakati pa cholowa cha ana a Israele ndiyo midzi makumi anai kudza isanu ndi itatu, ndi mabusa ao. 42Midzi iyi yonse inali nao mabusa ao pozungulira pao: inatero midzi iyi yonse. 43#Gen. 13.15Motero Yehova anawapatsa Israele dziko lonse adalumbiralo kuwapatsa makolo ao: ndipo analilandira laolao, nakhala m'mwemo. 44#Yos. 11.23Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaima munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m'manja mwao. 45#Yos. 23.14Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israele; zidachitika zonse.
Currently Selected:
YOSWA 21: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: