YouVersion Logo
Search Icon

AHEBRI 13

13
1 # Aro. 12.10 Chikondi cha pa abale chikhalebe. 2#Gen. 18.3; Mat. 25.35Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa. 3#Mat. 25.36Kumbukirani am'nsinga, monga am'nsinga anzao; ochitidwa zoipa, monga ngati inunso adatero nanu m'thupi. 4#1Ako. 6.9Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu. 5#Mat. 6.25, 34; Afi. 4.11Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu. 6#Mas. 118.6Kotero kuti tinena molimbika mtima,
Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa;
adzandichitira chiyani munthu?
7 # Aheb. 6.12; 13.7 Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao. 8#Yoh. 8.58; Chiv. 1.4Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthawi zonse. 9#Aef. 4.14; Aro. 14.17Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindula nazo. 10#1Ako. 9.13Tili nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema alibe ulamuliro wa kudyako.
11 # Eks. 29.14 Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa, ndi mkulu wa ansembe kulowa m'malo opatulidwa, chifukwa cha zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa. 12#Yoh. 19.17-18Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata. 13#1Pet. 4.14Chifukwa chake titulukire kwa Iye kunja kwa tsasa osenza tonzo lake. 14#Aheb. 11.10Pakuti pano tilibe mudzi wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo. 15#Mas. 50.14Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake. 16#Aro. 12.13Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo. 17#1Ate. 5.12; Mac. 20.26, 28Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.
18 # Akol. 4.3; 2Ako. 1.12 Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbu mtima chokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino. 19Ndipo ndikudandaulirani koposa kuchita ichi, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe.
20 # Aro. 12.10; Ezk. 37.24; Yoh. 10.11, 14; Aheb. 10.29 Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu, 21#Afi. 2.13akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.
22Koma ndidandaulira inu, abale, lolani mau a chidandauliro; pakutinso ndalembera inu mwachidule. 23#1Ate. 3.2Zindikirani kuti mbale wathu Timoteo wamasulidwa; pamodzi ndi iye, ngati akudza msanga, ndidzakuonani inu.
24 # Aheb. 7.17 Perekani moni kwa atsogoleri anu onse, ndi oyera mtima onse. Akupatsani moni iwo a ku Italiya.
25Chisomo chikhale ndi inu nonse, Amen.

Currently Selected:

AHEBRI 13: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in