YouVersion Logo
Search Icon

HABAKUKU 3

3
Pemphero la Habakuku
1Pemphero la Habakuku mneneri, pa Sigionoti.
2 # Mas. 85.6 Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha;
Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka,
pakati pa zaka mudziwitse;
pa mkwiyo mukumbukire chifundo.
3 # Deut. 33.2; Mas. 68.7 Mulungu anafuma ku Temani,
ndi Woyerayo kuphiri la Parani.
Ulemerero wake unaphimba miyamba,
ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.
4Ndi kunyezimira kwake kunanga kuunika;
anali nayo mitsitsi ya dzuwa yotuluka m'dzanja lake,
ndi komweko kunabisika mphamvu yake.
5Patsogolo pake panapita mliri,
ndi makala amoto anatuluka pa mapazi ake.
6Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi;
anapenya, nanjenjemeretsa amitundu;
ndi mapiri achikhalire anamwazika,
zitunda za kale lomwe zinawerama;
mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.
7Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka;
nsalu zotchinga za dziko la Midiyani zinanjenjemera.
8Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje?
Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi,
kapena ukali wanu panyanja,
kuti munayenda pa akavalo anu,
pa magaleta anu a chipulumutso?
9 # Mas. 78.15 Munapombosola uta wanu;
malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona.
Munang'amba dziko lapansi ndi mitsinje.
10Mapiri anakuonani, namva zowawa;
chigumula cha madzi chinapita;
madzi akuya anamveketsa mau ake,
nakweza manja ake m'mwamba.
11 # Yos. 10.12-13 Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao;
pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo.
Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.
12 # Yos. 10.11 Munaponda dziko ndi kulunda,
munapuntha amitundu ndi mkwiyo.
13 # Mas. 68.21 Munatulukira chipulumutso cha anthu anu,
chipulumutso cha odzozedwa anu;
munakantha mutu wa nyumba ya woipa,
ndi kufukula maziko kufikira m'khosi.
14Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake;
anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza;
kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika.
15 # Mas. 77.19 Munaponda panyanja ndi akavalo anu,
madzi amphamvu anaunjikana mulu.
16Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka,
milomo yanga inanthunthumira pamau,
m'mafupa mwanga mudalowa chivundi,
ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga;
kuti ndipumule tsiku lamsauko,
pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.
17Chinkana mkuyu suphuka,
kungakhale kulibe zipatso kumpesa;
yalephera ntchito ya azitona,
ndi m'minda m'mosapatsa chakudya;
ndi zoweta zachotsedwa kukhola,
palibenso ng'ombe m'makola mwao;
18 # Yob. 13.15; Yes. 61.10 koma ndidzakondwera mwa Yehova,
ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.
19 # Mas. 27.1 Yehova, Ambuye, ndiye mphamvu yanga,
asanduliza mapazi anga ngati a mbawala,
nadzandipondetsa pa misanje yanga.

Currently Selected:

HABAKUKU 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in