YouVersion Logo
Search Icon

ESTERE 1

1
Madyerero a Ahasuwero
1 # Ezr. 4.6; Dan. 9.1 Izi zinachitika masiku a Ahasuwero, ndiye Ahasuweroyo anachita ufumu kuyambira Indiya kufikira Kusi, pa maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri. 2#Neh. 1.1Masiku ajawo, pokhala Ahasuwero pa mpando wa ufumu wake uli m'chinyumba cha ku Susa, 3#Mrk. 6.21chaka chachitatu cha ufumu wake, anakonzera madyerero akalonga ake onse, ndi omtumikira; amphamvu a Persiya ndi Mediya, omveka ndi akalonga a maikowo anakhala pamaso pake, 4pamene anaonetsa zolemera za ufumu wake waulemu, ndi ulemerero wa ukulu wake woposa, masiku ambiri, ndiwo masiku zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu. 5Atatha masikuwa, mfumu inakonzera madyerero anthu onse okhala m'chinyumba cha ku Susa, akulu ndi ang'ono, masiku asanu ndi awiri, ku bwalo la munda wa maluwa wa ku chinyumba cha mfumu; 6panali nsalu zolenjeka zoyera, zabiriwiri, ndi zamadzi, zomangika ndi zingwe za thonje labafuta, ndi lofiirira, pa zigwinjiri zasiliva, ndi nsanamira zansangalabwi; makama anali a golide ndi siliva pa mayalidwe a miyala yofiira, ndi yoyera, ndi yoyezuka, ndi yakuda. 7Nawapatsa chakumwa m'zomwera zagolide, zomwerazo nzosiyanasiyana, ndi vinyo wachifumu anachuluka, monga mwa ufulu wa mfumu. 8Ndi mamwedwewo anali monga mwa lamulo; panalibe kukakamiza; pakuti mfumu idaikira akulu onse a nyumba yake motero, kuti achite monga momwe akhumba aliyense.
Vasiti akana kuoneka kumadyerero
9Vasiti yemwe, mkazi wamkulu, anakonzera akazi madyerero m'nyumba yachifumu ya mfumu Ahasuwero. 10Tsiku lachisanu ndi chiwiri, pokondwera mtima wa mfumu ndi vinyo, iye anauza Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, ndi Abagita, Zetara, ndi Karikasi, adindo asanu ndi awiriwo akutumikira pamaso pa mfumu Ahasuwero, 11abwere naye Vasiti mkazi wamkulu pamaso pa mfumu ndi korona wachifumu, kuonetsa anthu ndi akulu kukoma kwake; popeza anali wokongola maonekedwe ake. 12Koma Vasiti mkazi wamkuluyo anakana kudza pa mau a mfumu adamuuza adindowo; potero mfumu idapsa mtima ndithu, ndi mkwiyo wake unatentha m'kati mwake.
Vasiti achotsedwa
13 # Dan. 2.12; Mat. 2.1 Pamenepo mfumu inanena kwa eni nzeru, akudziwa za m'tsogolo, mfumu idafotero nao onse akudziwa malamulo ndi maweruzo, 14#Ezr. 7.14a pafupi naye ndiwo Karisena, Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena, ndi Memukana, akalonga asanu ndi awiri a Persiya ndi Mediya, openya nkhope ya mfumu ndi kukhala oyamba m'ufumu. 15Anati, Tidzachitanji naye mkazi wamkulu Vasiti monga mwa malamulo, popeza sanachite chomuuza mfumu Ahasuwero mwa adindo? 16Ndi Memukana anati, pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkulu sanalakwire mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m'maiko onse a mfumu Ahasuwero. 17#Aef. 5.33; Akol. 3.18Pakuti machitidwe awa a mkazi wamkuluyo adzabuka kufikira akazi onse, kupeputsa amuna ao pamaso pao; anthu akati, Mfumu Ahasuwero anati abwere naye Vasiti mkazi wamkulu pamaso pake, koma sanadze iye. 18Inde tsiku lomwelo akazi akulu a Persiya ndi Mediya, atamva machitidwe a mkazi wamkuluyo, adzatero nao momwemo kwa akalonga onse a mfumu. Ndi chipeputso ndi mkwiyo zidzachuluka. 19Chikakomera mfumu, atuluke mau achifumu pakamwa pake, nalembedwe m'malamulo a Apersiya ndi Amediya, angasinthike, kuti Vasiti asalowenso pamaso pa mfumu Ahasuwero; ndi mfumu aninkhe chifumu chake kwa mnzake womposa iye. 20#Aef. 5.33Ndipo mau amene adzaika mfumu akamveka m'ufumu wake wonse, (pakuti ndiwo waukulu), akazi onse adzachitira amuna ao ulemu, akulu ndi ang'ono. 21Ndipo mauwo anakonda mfumu ndi akalonga; ndi mfumu inachita monga mwa mau a Memukana, 22#Aef. 5.22, 24natumiza akalata kumaiko onse a mfumu, kudziko lililonse monga mwa chilembedwe chao, ndi kumtundu uliwonse monga mwa chinenedwe chao, kuti mwamuna aliyense akhale wamkulu m'nyumba yakeyake, nawabukitse monga mwa chinenedwe cha anthu a mtundu wake.

Currently Selected:

ESTERE 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy