YouVersion Logo
Search Icon

AEFESO 4

4
Umodzi wa iwo a chikhulupiriro
1 # Aef. 3.1; Akol. 1.10 Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao, 2#Mac. 20.19; Afi. 2.3ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi; 3#Akol. 3.14ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere. 4#1Ako. 12.4, 11Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m'chiyembekezo chimodzi cha maitanidwe anu; 5#1Ako. 1.13Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi, 6#1Ako. 8.6Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m'kati mwa zonse. 7#Aro. 12.3, 6Ndipo kwa yense wa ife chapatsika chisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Khristu.
8 # Mas. 68.18 Chifukwa chake anena,
M'mene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende,
naninkha zaufulu kwa anthu.
9 # Yoh. 6.33, 62 Koma ichi, chakuti, Anakwera, nchiyani nanga koma kuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko? 10#Mac. 1.9, 11Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse. 11#1Ako. 12.28Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; 12#1Ako. 12.7, 27kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu; 13#Akol. 1.28; 2.2-3kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu. 14#Aheb. 13.9Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa; 15#Zek. 8.16; 2Ako. 4.2; Akol. 1.18koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu; 16#Akol. 2.19kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.
Kusiyana kwa kuyera mtima kwa Chikhristu ndi mayendedwe oipa a akunja
17 # Aef. 2.1-2 Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'chitsiru cha mtima wao, 18#Aef. 2.12odetsedwa m'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yao; 19#Aro. 1.24, 26amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo. 20Koma inu simunaphunzira Khristu chotero, 21#Aef. 1.13ngatitu mudamva Iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye, monga choonadi chili mwa Yesu; 22#Aro. 6.6kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; 23#Akol. 3.10koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, 24#Akol. 3.10nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.
25 # Aro. 12.5; Aef. 4.15 Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake. 26#Mas. 37.8Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire, 27#Yak. 4.7ndiponso musampatse malo mdierekezi. 28#1Ate. 4.11Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa. 29#Akol. 3.8, 16Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva. 30#Yes. 63.10; Aef. 1.13Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe. 31#Akol. 3.8, 19Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse. 32#Mrk. 11.25; 1Pet. 3.8-9Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.

Currently Selected:

AEFESO 4: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in