YouVersion Logo
Search Icon

DANIELE 2

2
Nebukadinezara alota, Daniele ammasulira lotolo
1Chaka chachiwiri cha Nebukadinezara mfumu, Nebukadinezarayo analota maloto, ndi mzimu wake unavutika, ndi tulo take tidamwazikira. 2#Gen. 41.8Pamenepo mfumu inauza munthu aitane alembi, ndi openduza, ndi aula, ndi Ababiloni, amuululire mfumu maloto ake. Nalowa iwo, naimirira pamaso pa mfumu. 3Niti nao mfumu, Ndalota loto, nuvutika mzimu wanga kudziwa lotolo. 4#1Maf. 1.31Pamenepo Ababiloni anati kwa mfumu m'Chiaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwake. 5Niyankha mfumu, niti kwa Ababiloni, Chandichokera chinthuchi; mukapanda kundidziwitsa lotoli ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zanu zidzayesedwa dzala. 6Koma mukandidziwitsa lotoli, ndi kumasulira kwake, mudzalandira kwa ine mphatso, ndi mphotho, ndi ulemu waukulu; chifukwa chake mundidziwitse lotoli ndi kumasulira kwake. 7Nabwerezanso iwo kuyankha, nati, Mfumu ifotokozere anyamata ake lotoli, ndipo tidzaidziwitsa kumasulira kwake. 8Mfumu inayankha, niti, Ndidziwatu kuti mukunkhuniza dala, pakuona inu kuti chinthuchi chandichokera. 9Koma mukapanda kundidziwitsa lotoli, mlandu wanu ndi umodzi; popeza mwapanganiranatu mau onama ndi oipa, kuwanena pamaso panga, mpaka idzasanduka nyengo; chifukwa chake mundifotokozere lotoli, momwemo ndidzadziwa kuti mudzandidziwitsa kumasulira kwake komwe. 10Ababiloni anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu pa dziko lapansi wokhoza kuwulula mlandu wa mfumu; chifukwa chake palibe mfumu, mkulu, kapena wolamulira, wafunsira chinthu chotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Ababiloni ali onse. 11#Dan. 2.28; 5.11Pakuti chinthu achifuna mfumu nchapatali; ndipo palibe wina wokhoza kuchiwulula pamaso pa mfumu, koma milungu imene kwao sikuli pamodzi ndi anthu. 12Chifukwa chake mfumu inakwiya, nizaza kwambiri, nilamulira kuti awaphe anzeru onse m'Babiloni. 13M'mwemo chilamulirocho chidamveka, ndi eni nzeru adati aphedwe; anafunafunanso Daniele ndi anzake aphedwe. 14Pamenepo Daniele anabweza mau a uphungu wanzeru kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, adatulukawo kukapha eni nzeru a ku Babiloni; 15anayankha nati kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, Chilamuliro cha mfumu chifulumiriranji? Pamenepo Ariyoki anadziwitsa Daniele chinthuchi. 16Nalowa Daniele, nafunsa mfumu amuikire nthawi, kuti aululire mfumu kumasulira kwake.
17Pamenepo Daniele anapita kunyumba kwake, nadziwitsa anzake Hananiya, Misaele, ndi Azariya, chinthuchi; 18#Mat. 18.19kuti apemphe zachifundo kwa Mulungu wa Kumwamba pa chinsinsi ichi; kuti Daniele ndi anzake asaonongeke pamodzi ndi eni nzeru ena a ku Babiloni. 19#Num. 12.6Pamenepo chinsinsicho chinavumbulutsidwa kwa Daniele m'masomphenya a usiku. Ndipo Daniele analemekeza Mulungu wa Kumwamba. 20#Mas. 115.18; Yer. 32.19Daniele anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu kunthawi za nthawi, pakuti nzeru ndi mphamvu zili zake; 21#1Sam. 15.28; Yer. 32.19pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira. 22#Mas. 139.11-12; 1Yoh. 1.5Iye avumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye. 23#Dan. 2.18Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ichi tachifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu. 24Potero Daniele analowa kwa Ariyoki amene mfumu idamuika aononge eni nzeru a ku Babiloni; anamuka, natero naye, Usaononga eni nzeru a ku Babiloni, undilowetse kwa mfumu, ndipo ndidzaululira mfumu kumasulirako.
25Pamenepo Ariyoki analowa naye Daniele kwa mfumu mofulumira; natero nayo, Ndapeza munthu wa ana a ndende a Yuda, ndiye adzadziwitsa mfumu kumasulira kuja. 26Mfumu inayankha, niti kwa Daniele, amene dzina lake ndiye Belitesazara, Ukhoza kodi kundidziwitsa lotolo ndidalilota, ndi kumasulira kwake? 27Nayankha Daniele pamaso pa mfumu, nati, Chinsinsi inachitira liuma mfumu, angakhale anzeru, openduza, alembi, kapena alauli, sakhoza kuchiululira mfumu; 28#Gen. 40.8; 41.16koma kuli Mulungu Kumwamba wakuvumbulutsa zinsinsi; Iye ndiye wadziwitsa mfumu Nebukadinezara chimene chidzachitika masiku otsiriza. Loto lanu, ndi masomphenya a m'mtima mwanu pakama panu, ndi awa: 29#Dan. 2.22, 28Inu mfumu, maganizo anu analowa m'mtima mwanu muli pakama panu, akunena za icho chidzachitika m'tsogolomo; ndipo Iye amene avumbulutsa zinsinsi wakudziwitsani chodzachitikacho. 30#Gen. 40.8; 41.16Koma ine, chinsinsi ichi sichinavumbulutsidwa kwa ine chifukwa cha nzeru ndili nayo yakuposa wina aliyense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu. 31Inu mfumu munapenya ndi kuona fano lalikulu. Fanoli linali lalikulu, ndi kunyezimira kwake kunaposa; linali kuima popenyana ndi inu, ndi maonekedwe ake anali oopsa. 32#Dan. 2.38-45Fano ili tsono, mutu wake unali wagolide wabwino, chifuwa chake ndi manja ake zasiliva, mimba yake ndi chuuno chake zamkuwa, 33miyendo yake yachitsulo, mapazi ake mwina chitsulo mwina dongo. 34#Zek. 4.6; Mat. 21.44Munali chipenyere kufikira mwala unasemedwa popanda manja, umene unagunda fanoli pa mapazi ake okhala chitsulo ndi dongo, nuwaphwanya. 35#Yes. 2.2-3Pamenepo chitsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golide, zinapereka pamodzi, nizinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezekanso malo ao; ndi mwala udagunda fanowo unasanduka phiri lalikulu, nudzaza dziko lonse lapansi. 36Ili ndi loto; kumasulira kwake tsono tikufotokozerani mfumu. 37Inu mfumu ndinu mfumu ya mafumu, pakuti Mulungu wa Kumwamba anakupatsani ufumu, ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemu; 38ndipo paliponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga, m'dzanja lanu; nakuchititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolide. 39Ndi pambuyo pa inu padzauka ufumu wina wochepa ndi wanu, ndi ufumu wina wachitatu wamkuwa wakuchita ufumu pa dziko lonse lapansi. 40Ndi ufumu wachinai udzakhala wolimba ngati chitsulo, popeza chitsulo chiphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga chitsulo chiswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa. 41Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zake, mwina dongo la woumba, mwina chitsulo; ufumuwo udzakhala wogawanika, koma momwemo mudzakhala mphamvu ya chitsulo; popeza mudaona chitsulo chosanganizika ndi dongo. 42Ndi zala za mapazi, mwina chitsulo ndi mwina dongo, momwemo ufumuwo, mwina wolimba mwina wogamphuka. 43Ndi umo mudaonera chitsulo chosanganizika ndi dongo, iwo adzadzisokoneza ndi ana a anthu wamba; koma sadzaphatikizana, monga umo chitsulo sichimasanganizikana ndi dongo. 44#Dan. 4.3; Luk. 1.32-33Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire. 45#Yes. 28.16Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera chitsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golide; Mulungu wamkulu wadziwitsa mfumu chidzachitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwake kwakhazikika. 46#Mac. 10.25Pamenepo mfumu Nebukadinezara anagwa nkhope yake pansi, nalambira Daniele, nati amthirire nsembe yaufa ndi ya zonunkhira zokoma. 47#Dan. 2.28Mfumu inamyankha Daniele, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wovumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kuvumbulutsa chinsinsi ichi. 48#Dan. 2.6Pamenepo mfumu inasandutsa Daniele wamkulu, nimpatsa mphatso zazikulu zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babiloni; nakhala iye kazembe wamkulu wa anzeru onse a ku Babiloni. 49#Est. 2.19; Dan. 3.12Pamenepo Daniele anapempha mfumu, ndipo anaika Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, ayang'anire ntchito za dera la ku Babiloni. Koma Daniele anakhala m'bwalo la mfumu.

Currently Selected:

DANIELE 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

YouVersion uses cookies to personalize your experience. By using our website, you accept our use of cookies as described in our Privacy Policy