2 AKORINTO 4
4
Paulo alalikira Yesu yekhayekha
1 #
2Ako. 3.6
Chifukwa chake popeza tili nao utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifooka; 2#2Ako. 2.17; 5.11koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbu mtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu. 3#2Ako. 2.15-16Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika; 4#Yoh. 12.40; 2Ako. 4.6mwa amene mulungu wa nthawi yino ya pansi pano unachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire. 5#1Ako. 1.13, 23; 9.19Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Yesu Khristu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu. 6Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.
7 #
2Ako. 5.1; 12.9 Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife; 8#2Ako. 7.5ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; 9#Mas. 37.24olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka; 10#Agal. 6.17; Afi. 3.10nthawi zonse tilikusenzasenza m'thupi kufa kwake kwa Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi mwathu. 11#Aro. 8.36Pakuti ife amene tili ndi moyo tiperekeka kuimfa nthawi zonse, chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi lathu lakufa. 12#2Ako. 13.9Chotero imfa ichita mwa ife, koma moyo mwa inu. 13Koma pokhala nao mzimu womwewo wa chikhulupiriro, monga mwa cholembedwacho, ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula; ifenso tikhulupirira, chifukwa chake tilankhula; 14#Aro. 8.11podziwa kuti Iye amene anaukitsa Ambuye Yesu adzaukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiikapo pamodzi ndi inu. 15#2Ako. 1.6, 11Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu.
Chipatso cha kumva zowawa. Zosaoneka zilinganizidwa ndi zooneka
16 #
Aef. 3.16
Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku. 17#Mat. 5.12Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero; 18#Aro. 8.24popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.
Currently Selected:
2 AKORINTO 4: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: