YouVersion Logo
Search Icon

1 YOHANE 5

5
Za kukhulupirira Yesu ndi zotsatira zake
1 # Yoh. 1.12-13; 8.42 Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye. 2Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kuchita malamulo ake. 3#Mat. 11.30; Yoh. 14.15, 21, 23Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa. 4#Yoh. 16.33Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu. 5#1Ako. 15.57Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu? 6#Yoh. 19.34; 1Tim. 3.16Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi. 7Pakuti pali atatu akuchita umboni, 8Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi. 9#Mat. 3.16-17; Yoh. 8.17-18Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; chifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti anachita umboni za Mwana wake. 10#Aro. 8.16Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; iye wosakhulupirira Mulungu anamuyesa Iye wonama; chifukwa sanakhulupirira umboni wa Mulungu anauchita wa Mwana wake. 11#Yoh. 1.4; 1Yoh. 2.25Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake. 12Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo.
13 # 1Yoh. 1.1-2 Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.
Mphamvu ya kupemphera
14 # 1Yoh. 3.22 Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera; 15ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye. 16#Mat. 12.31-32; Yak. 5.14-15Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere. 17Chosalungama chilichonse chili uchimo; ndipo pali tchimo losati la kuimfa.
18 # Yak. 1.27; 1Yoh. 3.9 Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza. 19#Agal. 1.4Tidziwa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo. 20#Yes. 9.6; Yoh. 17.3; Mac. 20.28; Aro. 9.5; 1Yoh. 5.11Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha. 21#1Ako. 10.14Tiana, dzisungireni nokha kupewa mafano.

Currently Selected:

1 YOHANE 5: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in