1 AKORINTO 8:1-2
1 AKORINTO 8:1-2 BLPB2014
Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tili nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chitukumula, koma chikondi chimangirira. Ngati wina ayesa kuti adziwa kanthu sanayambe kudziwa monga ayenera kudziwa.





