YouVersion Logo
Search Icon

1 AKORINTO 16

16
Zopereka za kwa Akhristu a ku Yerusalemu
1 # Mac. 11.29; Agal. 2.10 Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso. 2#Mac. 20.7; Chiv. 1.10Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine. 3#2Ako. 8.19Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi akalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu. 4#Mac. 11.29; Agal. 2.10Ndipo ngati kuyenera kwa ine kupitanso, adzapita nane.
Za maulendo akudza, ndi malankhulano a Paulo
5 # Mac. 19.21 Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Masedoniya; pakuti ndidzapyola Masedoniya; 6#Aro. 15.24ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yachisanu kuti mukandiperekeze ine kumene kulikonse ndipitako. 7#Yak. 4.15Pakuti sindifuna kukuonani tsopano popitirira; pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye. 8Koma ndidzakhala ku Efeso kufikira Pentekoste. 9#Mac. 14.27Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.
10 # Mac. 19.22 Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine; 11#1Tim. 4.12chifukwa chake munthu asampeputse. Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale. 12#1Ako. 3.5Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichinali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene aona nthawi.
13 # Aef. 6.10; Afi. 1.27; 1Ate. 5.6 Dikirani, chilimikani m'chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani. 14#1Ako. 14.1Zanu zonse zichitike m'chikondi.
15 # 1Ako. 1.16; 2Ako. 9.1 Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choundukula cha Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima), 16#Aheb. 13.17kuti inunso muvomere otere, ndi yense wakuchita nao, ndi kugwiritsa ntchito. 17#2Ako. 11.9Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefanasi, ndi Fortunato, ndi Akaiko; chifukwa iwo anandikwaniritsa chotsalira chanu. 18Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu; chifukwa chake muzindikire otere.
19 # Aro. 16.3-5 Mipingo ya ku Asiya ikupatsani moni. Akupatsani moni ndithu inu mwa Ambuye, Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi Mpingo wa m'nyumba yao. 20#Aro. 16.16Akupatsani moni abale onse. Mupatsane moni ndi kupsompsona kopatulika.
21 # Akol. 4.18 Ndikupereka moni ine Paulo ndi dzanja langa. 22#Agal. 1.8-9Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye. 23#Aro. 16.20Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi inu. 24Chikondi changa chikhale ndi inu nonse mwa Khristu Yesu. Amen.

Currently Selected:

1 AKORINTO 16: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in