Afilipi 2:3-8
Afilipi 2:3-8 CCL
Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo. Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena. Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu: Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu, sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa. Koma anadzichepetsa kotheratu nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse. Ndipo pokhala munthu choncho anadzichepetsa yekha ndipo anamvera mpaka imfa yake, imfa yake ya pamtanda!