Numeri 16:30-32
Numeri 16:30-32 CCL
Koma Yehova akachita china chake chachilendo, nthaka nitsekula pakamwa pake ndi kuwameza iwo pamodzi ndi zonse zimene ali nazo, iwowa nʼkulowa mʼmanda ali moyo, pamenepo mudzazindikira kuti anthu amenewa ananyoza Yehova.” Atangotsiriza kuyankhula zimenezi, nthaka ya pamene anayimapo inagawikana ndipo dziko linatsekula pakamwa pake ndi kuwameza pamodzi ndi nyumba zawo ndi anthu onse a Kora ndi katundu wawo yense.





