Bible App logo
Search Icon

Yeremiya 3:13-14

Yeremiya 3:13-14 CCL

Ungovomera kulakwa kwako kuti unawukira Yehova Mulungu wako. Vomera kuti unayendayenda kukapembedza milungu yachilendo pansi pa mtengo uliwonse wogudira, ndiponso kuti sunandimvere,’ ” akutero Yehova. “Bwererani, ana osakhulupirika, pakuti ndine mbuye wanu,” akutero Yehova. “Ndinakusankhani, mmodzimmodzi kuchokera ku mudzi uliwonse ndiponso awiriawiri kuchokera ku banja lililonse.