Yeremiya 23:3-4
Yeremiya 23:3-4 CCL
“Pambuyo pake Ine mwini wakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku mayiko onse kumene ndinazibalalitsira ndi kuzibweretsanso ku msipu wawo. Kumeneko zidzaswana ndi kuchulukana. Ndidzazipatsa abusa amene adzaziweta, ndipo sizidzaopanso kapena kuchita mantha, ndipo palibe imene idzasochera,” akutero Yehova.





