Yeremiya 20:8-9
Yeremiya 20:8-9 CCL
Nthawi iliyonse ndikamayankhula, ndimafuwula kunena kuti, ziwawa kuno! Tikuwonongeka! Mawu anu Yehova andisandutsa chinthu chonyozeka ndipo ndimachitidwa chipongwe tsiku lonse. Koma ndikanena kuti, “Sindidzalalikiranso za Iye kapena kuyankhulanso mʼdzina lake,” mawu anu amayaka ngati moto mu mtima mwanga, amakhaladi ngati moto wotsekeredwa mʼmafupa anga. Ndapirira kusunga mawu anu mu mtima mwanga osawatulutsa, koma sindingathe kupirirabe.





