YouVersion Logo
Search Icon

Yesaya 52:14-15

Yesaya 52:14-15 CCL

Anthu ambiri atamuona anadzidzimuka, chifukwa nkhope yake inali itasakazika; sinalinso ngati ya munthu. Ndipo thupi lake linasakazika; silinalinso ngati la munthu. Momwemonso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye, ndipo mafumu adzatseka pakamwa pawo kusowa chonena chifukwa cha iye. Pakuti zinthu zimene iwo sanawuzidwepo, adzaziona, ndipo zimene sanazimvepo, adzazimvetsa.