Yesaya 43:6-7
Yesaya 43:6-7 CCL
Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’ ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’ Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali, ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi; onsewo amadziwika ndi dzina langa; ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga, ndinawawumba, inde ndinawapanga.”





