Yesaya 41:19-20
Yesaya 41:19-20 CCL
Mʼchipululu ndidzameretsa mkungudza, kasiya mchisu ndi mtengo wa Olivi. Mʼdziko lowuma ndidzaza mitengo ya payini, ya mkuyu ndi ya mlombwa, kuti anthu aone ndi kudziwa; inde, alingalire ndi kumvetsa, kuti Yehova ndiye wachita zimenezi; kuti Woyera wa Israeli ndiye anakonza zimenezi.





