Hagai 1:8-9
Hagai 1:8-9 CCL
Pitani ku mapiri ndipo mukatenge matabwa oti mudzamangire Nyumba yanga, kuti ndikondwere nayo ndi kulandiramo ulemu,” akutero Yehova. “Mumayembekezera zambiri, koma taonani mwapeza pangʼono pokha. Zimene munazibweretsa ku nyumba, Ine ndinazimwaza. Nʼchifukwa chiyani?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Chifukwa Nyumba yanga ikanali bwinja, pamene aliyense wa inu watanganidwa kumanga nyumba yake.





