Eksodo 10:13-14
Eksodo 10:13-14 CCL
Kotero Mose anakweza ndodo yake pa dziko la Igupto, ndipo Yehova anawutsa mphepo ya kummawa imene inawomba pa dziko usana ndi usiku wonse. Mmene kumacha nʼkuti mphepoyo itabweretsa dzombe. Dzombelo linafika pa dziko lonse la Igupto ndi kukhala dera lililonse la dzikolo. Dzombe lambiri ngati limenelo silinakhaleponso nʼkale lonse ndipo silidzakhalapo ngakhale mʼtsogolo.





