YouVersion Logo
Search Icon

Danieli 8:24-25

Danieli 8:24-25 CCL

Idzakhala yamphamvu kwambiri koma osati mphamvu za iyo yokha. Idzawononga koopsa ndipo idzapambana mu chilichonse chimene idzachite. Mfumuyi idzawononga anthu amphamvu ndi anthu oyera omwe. Chifukwa cha kuchenjera kwake chinyengo chidzachuluka pa nthawi ya ulamuliro wake, ndipo idzadzikuza kuposa onse. Pamene oyera mtima adzaona ngati kuti ali otetezedwa, iyo idzawononga ambiri ndi kuwukira ngakhale Mfumu ya mafumu. Komabe idzawonongedwa, koma osati ndi mphamvu za munthu.