Yohane 1
BL92
1
Umulungu wa Yesu Kristu
(Ahebri 1.5-13)
1PACIYAMBI panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu. 2Awa anali paciyambi kwa Mulungu, 3Zonse: zinalengedwa ndi iye; ndipo kopanda iye sikunalengedwa kanthu kali konse kolengedwa, 4Mwa iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu. 5Ndipo kuunikaku kunawala mumdima; ndi mdimawu sunakuzindikira.
Utumiki wa Yohane Mbatizi
(Yohane 1.29-34; Mateyu 3.1-17; Marko 1.1-11; Luka 3.1-23)
6Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lace ndiye Yohane. 7Iyeyu anadza mwa umboni kudzacita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye, 8iye sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukacita umboni wa kuunikaku.
Yesu Kristu kuunika koona kutifikira mwa kubadwa m'thupi
9Uku ndiko kuunika kweni kweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi. 10Anali m'dziko lapansi, ndi dziko linalengedwa ndi iye, koma dziko silinamzindikira iye. 11Anadza kwa zace za iye yekha, ndipo ace a mwini yekha sanamlandira iye. 12Koma onse amene anamlandira iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lace; 13amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi cifuniro ca thupi, kapena ndi cifuniro ca munthu, koma ca Mulungu. 14Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wace, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi cisomo ndi coonadi.
Umboni wa Yohane Mbatizi
(Mateyu 3.1-12; Marko 1.1-8; Luka 3.1-18)
15Yohane acita umboni za iye, napfuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; cifukwa anakhala woyamba wa ine. 16Cifukwa mwa kudzala kwace tinalandira ife tonse, cisomo cosinthana ndi cisomo. 17Cifukwa cilamulo cinapatsidwa mwa Mose; cisomo ndicoonadi zinadza mwa Yesu Kristu. 18Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa cifuwa ca Atate, Iyeyu anafotokozera.
19Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayudaanatuma kwa iye ansembe ndi alembi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani? 20Ndipo anabvomera, wosakana; nalola kuti, Sindine Kristu. 21Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye, Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai. 22Cifukwa cace anati kwa iye, Ndiwe yani? kuti tibwezere mau kwa iwo anatituma ife. Unena ciani za iwe wekha? 23Anati, 1 Ndine mau a wopfuula m'cipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo. 24Ndipo otumidwawo analia kwa Marisi. 25Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Kristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo? 26Yohane anawayankha, nati, 2 Ine ndibatiza ndi madzi; pakati pa inu paimirira amene simumdziwa, 273 ndiye wakudza pambuyo panga, amene sindiyenera kummasulira lamba la nsapato yace. 28Zinthu izi zinacitika m'Betaniya tsidya lija la Y ordano, pomwe analikubatiza Yohane.
29M'mawa mwace anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, 4 Onani Mwanawankhosa wa Mulungu 5 amene acotsa cimo lace la dziko lapasi! 306 Ndiye amene ndinati za iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine. 31Ndipo sindinamdziwa iye; koma kuti aonetsedwe kwa Israyeli, 7 cifukwa ca ici ndinadzaine kudzabatiza ndi madzi. 32Ndipo Yohane anacita umboni, nati, 8 Ndinaona Mzimu alikutsika kucokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa iye. 33Ndipo sindinamdziwa iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa iye, 9 yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera. 34Ndipo ndaona ine, ndipo ndacita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.
Ophunzira oyamba a Yesu
35M'mawa mwacenso analikuimirira Yohane ndi awiri a akuphunzira ace; 36ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, 10 Onani Mwanawankhosa wa Mulungu! 37Ndipo akuphunzira awiriwo anamva iye alinkulankhula, natsata Yesu. 38Koma Yesu anaceuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nao, Mufuna ciani? Ndipo anati kwa iye, Rabi (ndiko kunena posandulika, Mphunzitsi), mukhala kuti? 39Nanena nao, Tiyeni, mukaone, Pamenepo anadza naona kumene anakhala; nakhala ndi iye tsiku lomwelo; panali monga ora lakhumi. 40Andreya mbale wace wa Simoni Petro anali mmodzi wa awiriwo, anamva Yohane, namtsata iye. 41Anayamba iye kupeza mbale wace yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Kristu). 42Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; 11 udzachedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).
43M'mawa mwace anafuna kuturuka kunka ku Galileya, napeza Filipo, Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine. 44Koma Filipo anali wa ku Betsaida, mudzi wa Andreya ndi Petro. 45Filipo anapeza Natanayeli, nanena naye, iye 12 amene Mose analembera za iye m'cilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete. 46Natanayeli anati kwa iye, 13 Ku Nazarete nkutha kucokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone. 47Yesu anaona Natanayeli alinkudza kwa iye, nanena za iye, Onani, M-israyeli ndithu, mwa iye mulibe cinyengo! 48Natanayeli ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe. 49Natanayeli anayankha Iye, Rabi, 14 Inu ndinu Mwana wa Mulungu, 15 ndinu Mfumu ya Israyeli, 50Yesu anayankha nati kwa iye, Cifukwa ndinati kwa iwe kuti ndinakuona pansi pa mkuyu ukhulupirira kodi? udzaona zoposa izi. 51Ndipo ananena naye, Indetu, indetu, ndinena ndi Inu, 16 Mudzaona thambo lotseguka, ndi angeloa Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa munthu.

┬ęThe Bible Society of Malawi, 1992

Learn More About Buku Lopatulika 1992