Anthu a m'chigawo chachitatuchi ndidzaŵaika pa moto,
ndidzaŵayeretsa monga m'mene amayeretsera siliva.
Ndidzaŵayesa monga m'mene amayesera golide.
Tsono adzatama dzina langa mopemba,
Ine mwiniwake nkuŵayankha.
Ndidzanena kuti, ‘Ameneŵa ndi anthu anga.’
Iwowo adzati, ‘Chauta ndi Mulungu wathu.’ ”