1
Mk. 8:35
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa.
Compare
Explore Mk. 8:35
2
Mk. 8:36
Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse za pansi pano, iyeyo nkutaya moyo wake?
Explore Mk. 8:36
3
Mk. 8:34
Pambuyo pake Yesu adaitana khamu la anthu pamodzi ndi ophunzira aja kuti adze pafupi naye, ndipo adaŵauza kuti, “Munthu wofuna kutsana Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata.
Explore Mk. 8:34
4
Mk. 8:37-38
Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake? Tsono ngati munthu achita manyazi ndi Ine ndiponso ndi mau anga pamaso pa anthu ochimwa a makonoŵa amene ali osakhulupirika, ameneyo nanenso Mwana wa Munthune ndidzachita naye manyazi pamene ndidzabwera pamodzi ndi angelo oyera, ndili ndi ulemerero wa Atate anga.”
Explore Mk. 8:37-38
5
Mk. 8:29
Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” Petro adamuyankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja.”
Explore Mk. 8:29