1
Mk. 5:34
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere. Matenda anu atheretu.”
Compare
Explore Mk. 5:34
2
Mk. 5:25-26
Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Adaazunzika zedi ndi asing'anga ochuluka amene ankayesa kumuchiza. Mwakuti adaamwaza chuma chake chonse, komabe osapeza bwino konse. M'malo mwake matendawo analikunka nakulirakulira.
Explore Mk. 5:25-26
3
Mk. 5:29
Ndipodi nthaŵi yomweyo matenda a msambowo adaleka, mwiniwakeyo nkumva m'thupi mwake kuti matenda ake aja atha.
Explore Mk. 5:29
4
Mk. 5:41
Tsono adagwira mwanayo pa dzanja namuuza kuti, “Talita, kumi.” (Ndiye kuti, “Mtsikana iwe, ndikuti dzuka.”)
Explore Mk. 5:41
5
Mk. 5:35-36
Yesu akulankhulabe, kudafika anthu kuchokera kunyumba kwa mkulu uja. Adamuuza mkuluyo kuti, “Mwana uja watsirizika. Musaŵavutenso Aphunzitsiŵa.” Koma Yesu sadasamale zimene anthuwo ankanena. Adauza mkulu uja kuti, “Musaope ai, inu mungokhulupirira.”
Explore Mk. 5:35-36
6
Mk. 5:8-9
Adaatero chifukwa Yesu anali atanena kuti, “Mzimu woipawe, tuluka mwa munthuyu!” Tsono Yesu adamufunsa munthuyo kuti, “Dzina lako ndani?” Iye adayankha kuti, “Dzina langa ndine ‘Chigulu,’ chifukwa tilipo ochuluka.”
Explore Mk. 5:8-9