1
Mt. 27:46
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
BLY-DC
Tsono nthaŵi ili ngati 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eli, Eli, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?”
Compare
Explore Mt. 27:46
2
Mt. 27:51-52
Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika. Manda adatsekuka ndipo anthu a Mulungu ambiri amene anali atamwalira kale, adauka kwa akufa.
Explore Mt. 27:51-52
3
Mt. 27:50
Koma Yesu adafuulanso kwakukulu, napereka mzimu wake.
Explore Mt. 27:50
4
Mt. 27:54
Mkulu wa asilikali ndiponso amene anali naye polonda Yesu, ataona chivomezi chija ndi zina zonse zimene zidaachitika, adachita mantha kwambiri nati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.”
Explore Mt. 27:54
5
Mt. 27:45
Kuyambira pa 12 koloko masana mpaka pa 3 koloko, padaagwa mdima pa dziko lonse.
Explore Mt. 27:45
6
Mt. 27:22-23
Pilato adaŵafunsa kuti, “Nanga tsono ndichite naye chiyani Yesu, wotchedwa Khristuyu?” Anthu onse aja adati, “Apachikidwe pa mtanda!” Pilato adaŵafunsanso kuti, “Adalakwanji?” Koma anthu aja adafuula koposa kuti, “Apachikidwe pa mtanda!”
Explore Mt. 27:22-23