Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akulu, anakhala upo, napatsa asilikaliwo ndalama zambiri, nati, Kazinenani, kuti ophunzira ake anadza usiku, namuba Uja m'mene ife tinali m'tulo. Ndipo ngati ichi chidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhawa. Ndipo iwo analandira ndalamazo, nachita monga anawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe.