1
YESAYA 45:3
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
BLPB2014
ndipo ndidzakupatsa iwe chuma cha mumdima, ndi zolemera zobisika za m'malo am'tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israele.
Compare
Explore YESAYA 45:3
2
YESAYA 45:2
Ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzathyolathyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapichi achitsulo
Explore YESAYA 45:2
3
YESAYA 45:5-6
Ine ndili Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m'chuuno, ngakhale sunandidziwa; kuti anthu akadziwe kuchokera kumatulukiro a dzuwa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso.
Explore YESAYA 45:5-6
4
YESAYA 45:7
Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.
Explore YESAYA 45:7
5
YESAYA 45:22
Yang'anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko; pakuti Ine ndine Mulungu, palibe wina.
Explore YESAYA 45:22
6
YESAYA 45:1
Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Kirusi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, ndipo ndidzamasula m'chuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pake, ndi zipata sizidzatsekedwa
Explore YESAYA 45:1
7
YESAYA 45:23
Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m'kamwa mwanga m'chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.
Explore YESAYA 45:23
8
YESAYA 45:4
Ndakuitana iwe dzina lako, chifukwa cha Yakobo mtumiki wanga ndi Israele wosankhidwa wanga; ndakuonjezera dzina, ngakhale iwe sunandidziwa Ine.
Explore YESAYA 45:4