Chinkana mkuyu suphuka,
kungakhale kulibe zipatso kumpesa;
yalephera ntchito ya azitona,
ndi m'minda m'mosapatsa chakudya;
ndi zoweta zachotsedwa kukhola,
palibenso ng'ombe m'makola mwao;
koma ndidzakondwera mwa Yehova,
ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.