1
EKSODO 12:12-13
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
BLPB2014
Pakuti ndidzapita pakati pa dziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova. Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.
Compare
Explore EKSODO 12:12-13
2
EKSODO 12:14
Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.
Explore EKSODO 12:14
3
EKSODO 12:26-27
Ndipo kudzakhala, pamene ana anu adzanena ndi inu, Kutumikiraku muli nako nkutani? Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele m'Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.
Explore EKSODO 12:26-27
Home
Bible
Plans
Videos