Mulungu wa Israele anati,
Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine;
kudzakhala woweruza anthu molungama;
woweruza m'kuopa Mulungu.
Iye adzakhala ngati kuunika kwa m'mawa,
potuluka dzuwa, M'mawa mopanda mitambo;
pamene msipu uphuka kutuluka pansi,
chifukwa cha kuwala koyera, italeka mvula.