1
Mateyu 23:11
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Wamkulu pakati panu adzakhala wokutumikirani.
Compare
Explore Mateyu 23:11
2
Mateyu 23:12
Pakuti aliyense amene adzikuza adzachepetsedwa, ndipo aliyense amene adzichepetsa adzakuzidwa.
Explore Mateyu 23:12
3
Mateyu 23:23
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumapereka chakhumi cha timbewu tonunkhira ndi cha timbewu tokometsera chakudya. Koma mwasiya zofunikira kwambiri za mʼmalamulo monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika. Muyenera kuchita zomalizirazi komanso osasiya zoyambazo.
Explore Mateyu 23:23
4
Mateyu 23:25
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi achiphamaso! Mumayeretsa kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkatimo mwadzaza ndi dyera ndi kusadziretsa.
Explore Mateyu 23:25
5
Mateyu 23:37
“Haa! Yerusalemu, Yerusalemu, iwe amene umapha aneneri ndi kugenda miyala amene atumidwa kwa iwe, kawirikawiri ndimafuna kusonkhanitsa ana ako, monga nkhuku imasonkhanitsira ana ake pansi pa mapiko ake, koma iwe sunafune.
Explore Mateyu 23:37
6
Mateyu 23:28
Chimodzimodzinso, kunja mumaoneka kwa anthu kuti ndinu olungama koma mʼkatimo ndinu odzaza ndi chinyengo ndi zoyipa zina.
Explore Mateyu 23:28