1
Levitiko 26:12
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Ine ndidzayendayenda pakati panu ndipo ndidzakhala Mulungu wanu. Inu mudzakhala anthu anga.
Compare
Explore Levitiko 26:12
2
Levitiko 26:4
ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake. Nthaka yanu idzabala zokolola zake, ndipo mitengo ya mʼmunda idzabala zipatso zake.
Explore Levitiko 26:4
3
Levitiko 26:3
“ ‘Mukamayenda motsata malangizo anga ndi kumvera mosamalitsa malamulo anga
Explore Levitiko 26:3
4
Levitiko 26:6
“ ‘Ndidzabweretsa mtendere mʼdziko lanu, ndipo muzidzagona popanda wokuopsezani. Ndidzachotsa nyama zakuthengo zoopsa mʼdziko mwanu, ndipo mʼdzikomo simudzakhala nkhondo.
Explore Levitiko 26:6
5
Levitiko 26:9
“ ‘Ndidzakukumbukirani ndi kukupatsani ana ambiri ndi kukuchulukitsani. Ndidzasunga pangano langa ndi inu.
Explore Levitiko 26:9
6
Levitiko 26:13
Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti musakhalenso akapolo a Aigupto. Ndinadula mipiringidzo ya goli lanu ndi kukuthandizani kuti muziyenda momasuka.
Explore Levitiko 26:13
7
Levitiko 26:11
Ndidzakhala pakati panu, ndipo sindidzayipidwa nanu.
Explore Levitiko 26:11
8
Levitiko 26:1
“ ‘Musadzipangire mafano ndipo musayimike chifanizo chosema kapena mwala woti mudzipembedza. Musayike mwala wosema mʼdziko mwanu kuti muziwugwadira. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Explore Levitiko 26:1
9
Levitiko 26:10
Mudzakhala mukudyabe chakudya chogonera ndipo mudzachotse chakudyacho mʼnkhokwe kuti mupezemo malo woyika chakudya china chatsopano.
Explore Levitiko 26:10
10
Levitiko 26:8
Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga.
Explore Levitiko 26:8
11
Levitiko 26:5
Mudzakhala mukupuntha tirigu mpaka nthawi yothyola mphesa, ndipo mudzakhala mukuthyola mphesa mpaka nthawi yodzala. Mudzadya chakudya chanu mpaka kukhuta ndipo mudzakhala mʼdziko lanu mwamtendere.
Explore Levitiko 26:5
12
Levitiko 26:7
Mudzapirikitsa adani anu, ndipo mudzawagonjetsa ndi lupanga pamaso panu.
Explore Levitiko 26:7
13
Levitiko 26:2
“ ‘Muzisunga Masabata anga ndipo muzilemekeza malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova.
Explore Levitiko 26:2