1
Yeremiya 8:22
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa? Kodi kumeneko kulibe singʼanga? Nanga chifukwa chiyani mabala a anthu anga sanapole?
Compare
Explore Yeremiya 8:22
2
Yeremiya 8:4
“Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti: “ ‘Kodi anthu akagwa sangadzukenso? Munthu akasochera kodi sangathe kubwereranso?
Explore Yeremiya 8:4
3
Yeremiya 8:7
Mbalame yotchedwa kakowa ija imadziwa nthawi yake mlengalenga. Koma nkhunda, namzeze ndi chingalu zimadziwa nthawi yonyamukira ulendo, koma anthu anga sadziwa malamulo a Yehova.
Explore Yeremiya 8:7
4
Yeremiya 8:6
Ine ndinatchera khutu kumvetsera koma iwo sanayankhulepo zoona. Palibe woyipa amene analapapo zoyipa zake, nʼkumati, ‘Ine ndachita chiyani?’ Aliyense akutsatira njira yake ngati kavalo wothamangira nkhondo.
Explore Yeremiya 8:6
5
Yeremiya 8:9
Anthu anzeru achita manyazi; athedwa nzeru ndipo agwidwa. Iwo anakana mawu a Yehova. Nanga tsono nzeru zawo ziwapinduliranji?
Explore Yeremiya 8:9