1
Yesaya 42:6-7
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
“Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama; ndikugwira dzanja ndipo ndidzakuteteza. Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthu ndi kuwunika kwa anthu a mitundu ina. Udzatsekula maso a anthu osaona, udzamasula anthu a mʼndende ndi kutulutsa mʼndende anthu okhala mu mdima.
Compare
Explore Yesaya 42:6-7
2
Yesaya 42:8
“Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo! Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense kapena matamando anga kwa mafano.
Explore Yesaya 42:8
3
Yesaya 42:1
“Nayu mtumiki wanga, amene ndimamuchirikiza, amene ndamusankha, amenenso ndimakondwera naye. Ndayika Mzimu wanga mwa Iyeyo, ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.
Explore Yesaya 42:1
4
Yesaya 42:3-4
Bango lophwanyika sadzalithyola, ndipo moto wozilala sadzawuzimitsa. Motero adzaonetsa kuti chilungamo ndicho choonadi; sadzafowoka kapena kukhumudwa mpaka atakhazikitsa chilungamo pa dziko lapansi, ndi mpaka mayiko a mʼmbali mwa nyanja atafika poyembekezera malangizo ake.”
Explore Yesaya 42:3-4
5
Yesaya 42:16
Ndidzatsogolera anthu osaona mʼmisewu imene sanayidziwe, ndidzawatsogolera mʼnjira zimene sanayendepo; ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwawo kuti ukhale kuwala ndipo ndidzasalaza malo osalala. Zimenezi ndizo ndidzachite; sindidzawataya.
Explore Yesaya 42:16
6
Yesaya 42:9
Taonani, zinthu zimene ndinalosera kale zachitikadi, ndipo ndikuwuzani zinthu zatsopano; zinthuzo zisanaonekere Ine ndakudziwitsani.”
Explore Yesaya 42:9