1
Yesaya 35:10
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera. Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba; kumeneko adzakondwa mpaka muyaya. Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe, ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
Compare
Explore Yesaya 35:10
2
Yesaya 35:3-4
Limbitsani manja ofowoka, limbitsani mawondo agwedegwede; nenani kwa a mitima yamantha kuti; “Limbani mtima, musachite mantha; Mulungu wanu akubwera, akubwera kudzalipsira; ndi kudzabwezera chilango adani anu; akubwera kudzakupulumutsani.”
Explore Yesaya 35:3-4
3
Yesaya 35:8
Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu; ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika. Anthu odetsedwa sadzayendamo mʼmenemo; zitsiru sizidzasochera mʼmenemo.
Explore Yesaya 35:8
4
Yesaya 35:5
Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyanso ndipo makutu a anthu osamva adzatsekuka.
Explore Yesaya 35:5
5
Yesaya 35:6
Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala, ndipo osayankhula adzayimba mokondwera. Akasupe adzatumphuka mʼchipululu ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma
Explore Yesaya 35:6