Pamenepo opulumuka mwa inu adzandikumbukira ku mayiko kumene anatengedwa ukapolo. Ndidzawamvetsa chisoni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo ndi kundipandukira kuja ndiponso chifukwa kuti anayika mtima wawo pa mafano. Choncho adzachita okha manyazi chifukwa cha zoyipa zimene ankachita ndi miyambo yonyansa imene ankatsata.