1
Ezekieli 34:16
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Ndidzafunafuna zotayika ndi kubweza zosochera. Ndidzamanga mabala a zopweteka ndi kulimbikitsa zofowoka. Koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaweta nkhosazo mwachilungamo.
Compare
Explore Ezekieli 34:16
2
Ezekieli 34:12
Monga mʼbusa amanka nafunafuna nkhosa zake pamene zina zabalalikira kutali, moteronso Ine ndidzafunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa kuchoka kumalo onse kumene zinabalalikira pa nthawi yankhungu ndi mdima.
Explore Ezekieli 34:12
3
Ezekieli 34:11
“ ‘Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti, mwini wakene ndidzazifunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira.
Explore Ezekieli 34:11
4
Ezekieli 34:15
Ine mwini wake ndidzaziweta nkhosa zanga ndi kuzilola kuti zipumule. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Explore Ezekieli 34:15
5
Ezekieli 34:31
Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimazidyetsa. Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse.’ ”
Explore Ezekieli 34:31
6
Ezekieli 34:2
“Iwe mwana wa munthu, yankhula mawu oyimba mlandu abusa a Israeli. Lengeza ndipo uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Tsoka kwa abusa a Israeli amene mumangodzisamala nokha! Kodi abusa sayenera kusamalira nkhosa?
Explore Ezekieli 34:2