1
Aefeso 6:12
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga.
Compare
Explore Aefeso 6:12
2
Aefeso 6:18
Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.
Explore Aefeso 6:18
3
Aefeso 6:11
Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana.
Explore Aefeso 6:11
4
Aefeso 6:13
Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu.
Explore Aefeso 6:13
5
Aefeso 6:16-17
Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo. Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu.
Explore Aefeso 6:16-17
6
Aefeso 6:14-15
Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa. Valani Uthenga Wabwino wamtendere ku mapazi anu ngati nsapato.
Explore Aefeso 6:14-15
7
Aefeso 6:10
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu.
Explore Aefeso 6:10
8
Aefeso 6:2-3
“Lemekeza abambo ndi amayi ako.” Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, “zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi.”
Explore Aefeso 6:2-3
9
Aefeso 6:1
Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera.
Explore Aefeso 6:1
Home
Bible
Plans
Videos