1
Mlaliki 7:9
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
CCL
Usamafulumire kukwiya mu mtima mwako, pakuti mkwiyo ndi bwenzi la zitsiru.
Compare
Explore Mlaliki 7:9
2
Mlaliki 7:14
Pamene zinthu zili bwino, sangalala; koma pamene zinthu sizili bwino, ganizira bwino: Mulungu ndiye anapanga nthawi yabwinoyo, ndiponso nthawi imene si yabwinoyo. Choncho munthu sangathe kuzindikira chilichonse cha mʼtsogolo mwake.
Explore Mlaliki 7:14
3
Mlaliki 7:8
Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake, ndipo kufatsa nʼkwabwino kupambana kudzikuza.
Explore Mlaliki 7:8
4
Mlaliki 7:20
Palibe munthu wolungama pa dziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha ndipo sachimwa.
Explore Mlaliki 7:20
5
Mlaliki 7:12
Nzeru ndi chitetezo, monganso ndalama zili chitetezo, koma phindu la chidziwitso ndi ili: kuti nzeru zimasunga moyo wa munthu amene ali nazo nzeruzo.
Explore Mlaliki 7:12
6
Mlaliki 7:1
Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino, ndipo tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.
Explore Mlaliki 7:1
7
Mlaliki 7:5
Kuli bwino kumva kudzudzula kwa munthu wanzeru kusiyana ndi kumvera mayamiko a zitsiru.
Explore Mlaliki 7:5
8
Mlaliki 7:2
Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro kusiyana ndi kupita ku nyumba yamadyerero: Pakuti imfa ndiye mathero a munthu aliyense; anthu amoyo azichisunga chimenechi mʼmitima mwawo.
Explore Mlaliki 7:2
9
Mlaliki 7:4
Mtima wa munthu wanzeru nthawi zonse umalingalira za imfa, koma mitima ya zitsiru imalingalira za chisangalalo.
Explore Mlaliki 7:4