Yehova akunena kuti
“Nthawi ikubwera pamene mlimi wotipula adzapyola wokolola
ndipo woponda mphesa adzapyola wodzala mbewu.
Mapiri adzachucha vinyo watsopano
ndi kuyenderera pa zitunda zonse.
Ndidzawabwezeranso pabwino anthu anga Aisraeli;
mizinda imene inali mabwinja idzamangidwanso ndipo azidzakhalamo.
Adzalima minda ya mpesa ndipo adzamwa vinyo wake;
adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.