Chapa ya Youversion
Ikoni ya Utafutaji

AGALATIYA 6

6
Malangizo otsiriza, kulawirana
1 # 1Ako. 10.12; 2Ate. 3.15 Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso. 2#Aro. 15.1Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu. 3#Aro. 12.3Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha. 4#2Ako. 13.5Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina. 5#1Ako. 3.8Pakuti yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.
6Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m'zonse zabwino. 7#Luk. 16.25Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. 8#Aro. 8.13Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha. 9#1Ako. 15.58Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka. 10#1Ate. 5.15Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.
11Taonani, malembedwe akuluwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini. 12#Agal. 5.11Onse amene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukakamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu. 13Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m'thupi lanu. 14#Aro. 6.6; Afi. 3.3, 7-8Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi. 15#Agal. 5.6; Akol. 3.11Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano. 16Ndipo onse amene atsatsa chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu. 17#2Ako. 11.23Kuyambira tsopano palibe munthu andivute, pakuti ndili nayo ine m'thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu.
18Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu, abale. Amen.

Iliyochaguliwa sasa

AGALATIYA 6: BLPB2014

Kuonyesha

Shirikisha

Nakili

None

Je, ungependa vivutio vyako vihifadhiwe kwenye vifaa vyako vyote? Jisajili au ingia