AGALATIYA 5
5
Asunge ufulu wa Chikhristu
1 #
Yoh. 8.32, 36; Mac. 15.10 Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo. 2#Mac. 15.1Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu. 3#Aro. 2.25Ndichitanso umboni kwa munthu yense wolola amdule, kuti ali wamangawa kuchita chilamulo chonse. 4#Aro. 9.31-32Mulibe kanthu ndi Khristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana nacho chisomo. 5#Aro. 8.24-25Pakuti ife mwa Mzimu, kuchokera m'chikhulupiriro, tilindira chiyembekezo cha chilungamo. 6#Agal. 3.28; Yak. 2.18, 20, 22Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi. 7#Agal. 3.1Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere choonadi? 8#Agal. 1.6Kukopa kumene sikuchokera kwa Iye anakuitanani. 9#1Ako. 5.6Chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse. 10#Agal. 1.7Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakuvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza chitsutso chake. 11#1Ako. 1.23; 15.30Koma ine, abale, ngati ndilalikiranso mdulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo chikhumudwitso cha mtanda chidatha. 12Mwenzi atadzidula, iwo akugwedezetsani inu.
13 #
1Ako. 8.9; 9.19 Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo. 14#Mat. 22.39Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. 15Koma ngati mulumana ndi kudyana, chenjerani mungaonongane.
Ntchito za thupi ndi zipatso za Mzimu
16 #
Aro. 8.14
Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi. 17#Aro. 7.23Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite. 18#Aro. 8.14Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo. 19#1Ako. 3.3Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, 20kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, 21#Aef. 5.5njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu. 22#Yoh. 15.2Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, 23chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo. 24#Aro. 6.6Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake.
25 #
Aro. 8.4-5
Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende. 26#Afi. 2.3Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.
Iliyochaguliwa sasa
AGALATIYA 5: BLPB2014
Kuonyesha
Shirikisha
Nakili
Je, ungependa vivutio vyako vihifadhiwe kwenye vifaa vyako vyote? Jisajili au ingia
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: