1
MATEYU 27:46
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
BLPB2014
Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau akulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?
Linganisha
Chunguza MATEYU 27:46
2
MATEYU 27:51-52
Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha m'Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika; ndi manda anatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka
Chunguza MATEYU 27:51-52
3
MATEYU 27:50
Ndipo Yesu, pamene anafuula ndi mau akulu, anapereka mzimu wake.
Chunguza MATEYU 27:50
4
MATEYU 27:54
Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu.
Chunguza MATEYU 27:54
5
MATEYU 27:45
Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.
Chunguza MATEYU 27:45
6
MATEYU 27:22-23
Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Khristu? Onse anati, Apachikidwe pamtanda. Ndipo iye anati, Chifukwa ninji? Anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsa kopambana, Apachikidwe pamtanda.
Chunguza MATEYU 27:22-23
Nyumbani
Biblia
Mipango
Video