Chapa ya Youversion
Ikoni ya Utafutaji

2 AKORINTO 12

12
Masomphenya a Paulo ndi munga m'thupi lake
1Ndiyenera kudzitamandira, kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza kumasomphenya ndi mavumbulutso a Ambuye. 2#Mac. 22.17Ndidziwa munthu wa mwa Khristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwachitatu. 3Ndipo ndidziwa munthu wotereyo (ngati m'thupi, ngati wopanda thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), 4#Luk. 23.43kuti anakwatulidwa kunka ku Paradaiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula. 5#2Ako. 11.30Chifukwa cha wotereyo ndidzadzitamandira; koma chifukwa cha ine ndekha sindidzadzitamandira, koma m'zofooka zanga. 6Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira, sindidzakhala wopanda nzeru; pakuti ndidzanena choonadi; koma ndileka, kuti wina angandiwerengere ine koposa kumene andiona ine, kapena amva za ine. 7#Agal. 4.13-14Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa. 8#Mat. 26.44Za ichi ndinapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine. 9#2Ako. 11.30; 1Pet. 4.14Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m'ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine. 10#Aro. 5.3; 2Ako. 13.4Chifukwa chake ndisangalala m'mafooko, m'ziwawa, m'zikakamizo, m'mazunzo, m'zipsinjiko, chifukwa cha Khristu; pakuti pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.
Kusadzikonda kwa Paulo
11 # 2Ako. 11.5; Aef. 3.8 Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewera ndi atumwi oposatu m'kanthu konse, ndingakhale ndili chabe. 12#Aro. 15.18-19Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati pa inu, m'chipiriro chonse, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi zamphamvu. 13#1Ako. 1.7; 9.12Pakuti kuli chiyani chimene munachepetsedwa nacho ndi Mipingo yotsala ina, ngati si ichi kuti ine ndekha sindinasaukitsa inu? Ndikhululukireni choipa ichi. 14#Mac. 20.33; 2Ako. 13.1Taonani, nthawi yachitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amai, koma atate ndi amai kuunjikira ana. 15#Afi. 2.17Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa? 16#2Ako. 11.9Koma kukhale kotero; ine sindinalemetsa inu; koma pokhala wochenjera ine, ndinakugwirani ndi chinyengo. 17#2Ako. 7.2Kodi wina wa iwo ndinawatuma kwa inu, ndinakuchenjererani naye kodi? 18#2Ako. 8.6, 16, 22Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayenda naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsata mapazi omwewo kodi?
Malangizo otsiriza, zolawirana
19 # 1Ako. 10.33; 2Ako. 5.12 Mumayesa tsopano lino kuti tilikuwiringula kwa inu. Tilankhula pamaso pa Mulungu mwa Khristu. Koma zonse, okondedwa, zili za kumangirira kwanu. 20#1Ako. 4.21Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso; 21#2Ako. 2.1, 4; 13.2kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.

Iliyochaguliwa sasa

2 AKORINTO 12: BLPB2014

Kuonyesha

Shirikisha

Nakili

None

Je, ungependa vivutio vyako vihifadhiwe kwenye vifaa vyako vyote? Jisajili au ingia