Chapa ya Youversion
Ikoni ya Utafutaji

1 AKORINTO 2

2
Ulalikidwe wa Paulo
1 # 1Ako. 1.17 Ndipo ine, abale, m'mene ndinadza kwa inu, sindinadza ndi kuposa kwa mau, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu chinsinsi cha Mulungu. 2#Agal. 6.14Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu, koma Yesu Khristu, ndi Iye wopachikidwa. 3#2Ako. 10.1, 10Ndipo ine ndinakhala nanu mofooka ndi m'mantha, ndi monthunthumira mwambiri. 4#Aro. 15.19; 1Ako. 1.17Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu; 5#2Ako. 4.7kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.
6 # 1Ako. 1.20; Aef. 4.13 Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi yino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi yino ya pansi pano, amene alinkuthedwa; 7#Aef. 3.5, 9koma tilankhula nzeru ya Mulungu m'chinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu anaikiratu, pasanakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu, 8#Luk. 23.34imene saidziwa mmodzi wa akulu a nthawi ya pansi pano: pakuti akadadziwa sakadapachika Mbuye wa ulemerero; 9#Yes. 64.4koma monga kulembedwa,
Zimene diso silinaziona, ndi khutu silinazimva,
nisizinalowa mu mtima wa munthu,
zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.
10 # 1Pet. 4.11 Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe. 11#Aro. 11.33-34Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu. 12#Aro. 8.15Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu. 13#1Ako. 1.17Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu. 14#Mat. 16.23; Aro. 8.5-7Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu. 15#1Yoh. 4.1Koma iye amene ali wauzimu ayesa zonse, koma iye yekha sayesedwa ndi mmodzi yense. 16#Yes. 40.13; Yoh. 15.15Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize Iye? Koma ife tili nao mtima wa Khristu.

Iliyochaguliwa sasa

1 AKORINTO 2: BLPB2014

Kuonyesha

Shirikisha

Nakili

None

Je, ungependa vivutio vyako vihifadhiwe kwenye vifaa vyako vyote? Jisajili au ingia