1 AKORINTO 12:8-10
1 AKORINTO 12:8-10 BLPB2014
Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzake mau a chidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo: kwa wina chikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa Mzimu mmodziyo; ndi kwa wina machitidwe a mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundumitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.


