1 AKORINTO 10
10
Tisayese dala Mulungu monga Israele
1 #
Eks. 13.21-22; 14.22 Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse; 2nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m'nyanja, 3#Eks. 16.15-35nadya onse chakudya chauzimu chimodzimodzi; 4#Eks. 17.6namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Khristu. 5#Num. 14.29, 32, 35Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwera nao; pakuti anamwazika m'chipululu. 6Koma zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka. 7#Eks. 32.6Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera. 8#Num. 25.1-9Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu. 9#Num. 21.5-9Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija. 10#Num. 14.2-29Kapena musadandaula, monga ena a iwo anadandaula, naonongeka ndi woonongayo. 11#Aro. 15.4Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife. 12#Aro. 11.20Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang'anire kuti angagwe. 13#2Pet. 2.9Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
Za kupembedza mafano, za kuyanjana ndi ziwanda
14Chifukwa chake, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano. 15Ndinena monga kwa anzeru; lingirirani inu chimene ndinena. 16#Mat. 26.26-28Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi? 17#Aro. 12.5Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako kumkate umodzi. 18#Lev. 7.15Tapenyani Israele monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe chiyanjano ndi guwa la nsembe? 19#1Ako. 8.4Ndinena chiyani tsono? Kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chili kanthu? Kapena kuti fano lili kanthu kodi? 20#Deut. 32.17Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda. 21#2Ako. 6.15-16Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda. 22#Deut. 32.21Kapena kodi tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye?
Mkhristu ndiye mfulu koma wosamalira ena
23 #
1Ako. 6.12
Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse. 24#Aro. 15.1-2Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake. 25#1Tim. 4.4Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu chifukwa cha chikumbu mtima; 26#Mas. 24.1pakuti dziko lapansi lili la Ambuye, ndi kudzala kwake. 27#Luk. 10.7Ngati wina wa osakhulupirira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye chomwe chiikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, chifukwa cha chikumbu mtima. 28#1Ako. 8.10Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbu mtima. 29#Aro. 14.16Ndinena chikumbu mtima, si cha iwe mwini, koma cha winayo; pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi chikumbu mtima cha wina? 30Ngati ine ndilandirako mwachisomo, ndinenezedwa bwanji chifukwa cha ichi chimene ndiyamikapo? 31#Akol. 3.17Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. 32#Aro. 14.13Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Agriki, kapena Mpingo wa Mulungu; 33#Aro. 15.2monga inenso ndikondweretsa onse m'zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha unyunjiwo, kuti apulumutsidwe.
Iliyochaguliwa sasa
1 AKORINTO 10: BLPB2014
Kuonyesha
Shirikisha
Nakili
Je, ungependa vivutio vyako vihifadhiwe kwenye vifaa vyako vyote? Jisajili au ingia
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi

: