Logo de YouVersion
Icono de búsqueda

Matayo 9

9
Yesu wamlamicha mundhu ovuwala
Maluko 2:1-12; Luka 5:17-26
1Yesu wadakwela mboti, wadayomboka nyanja ni wadabwela kumujhi kwake. 2Kumeneko adampelekela mundhu ovuwala uyo wadagona pachitala. Yesu yapo wadaona chikulupi chao, wadamkambila mundhu yujha ovulala, “Limba mtima mwana wanga! Walekeledwa machimo yako!”
3Akumojhi awoyaluza mathauko amakambilana achinawene, “Mundhu uyu wamchita chipongwe Mnungu!”
4Yesu wadajhiwa ivo amakambilana, wadafunjha, “Bwanji, ndande yanji mkambilana voipa? 5Liti lili lopepuka, kukamba, ‘Walekeleledwa machimo yako,’ kapina kukamba, ‘Ima uyende?’ 6Chipano nifuna mjhiwe kuti Mwana wa Mundhu wali nilamulo mujhiko lakulekelela machimo ya wandhu.” Pamwepo wadamkambila yujha mundhu ovulala, “Ima, tenga chitala chako, ujhipita kukhomo kwako!”
7Pampajha Yujha mundhu wadavula wadaima ni kupita kukhomo lake. 8Wandhu onjhe yapo adapenya yameneyo adaopa, adamlemekeza Mnungu uyo waapacha wandhu ulamulilo.
Yesu wamtana Matayo
Maluko 2:13-17; Luka 5:27-32
9Yesu wadachokapo pamenepo, ni yapo wamachoka wadamuona mundhu mwina wolandila malipilo uyo watanidwa Matayo, wakhala mnyumba ya malipilo. Yesu wadamtana ni kumkambila, “Nichate.”
Matayo wadaima ni kumchata.
10Yesu yapo wamadya chakudya mnyumba ya Matayo, olandila malipilo ambili ni amachimo adajha kudya chakudya pamojhi ni Yesu ni oyaluzidwa wake. 11Afalisayo yapoadaona yameneyo, wadaafunjha oyaluzidwa a Yesu, “Ndande yanjhi oyaluza wanu wakudya pamojhi ni olandila malipilo ni amachimo?”
12Yesu yapo wadavela yameneyo, wadakamba, “Wandhu yawo asangalala siafuna singanga nambho odwala. 13Nambho mpite mkajhiyaluze mate ya mawu yaya, Nifuna lisungu, osati njhembe. Sinidajhe kwatana wandhu abwino nambho amachimo.”
Yesu wafunjhidwa nghani zomanga
Maluko 2:18-22; Luka 5:33-39
14Oyaluzidwa a Yohana Mbatizi adamjhela Yesu, adamfunjha, “Ndande yanji ife ni Mafalisayo timanga, nambho oyaluzidwa wanu siamanga?”
15Yesu wadayangha, “Bwanji, anyiwajha atanidwa kuukwati sakhale bwanji ni chisoni ni kusiya kudya ni kumwa? Saakhoza kusiya. Nambho ndhawi siijhe okwata yapo siwachochedwe pakati pawo, pamenepo ndeyapo sakhale ni chisoni kusiya kudya ni kumwa.”
16“Wandhu sasoka chigamba cha chipano ni kuchiika panjhalu ya kale. Ndande chigamba chimenecho siching'ambe njhalu ya kale ni pajha pang'ambika sipakule kupitilila poyamba. 17Wala wandhu saathila divai yachipano mmatumba yolema ya vikwetu va mbelele. Akachita chimwecho, matumba yameneyo siyasweke ni divai simwazike. Nambho, wandhu ayika divai yachipano matumba ya vikwetu vachipano, ni vonjhe viwili sivikhale bwino.”
Mwali wa wamkulu ni wamkazi mmojhi alamichidwa
Maluko 5:21-43; Luka 8:40-56
18Yesu yapo wamakamba yameneyo, wamkulu mmojhi wa Ayahudi wadamgwadila, ni kukamba, “Mwana wanga wa mwalilila chipano yapa. Nambho, nikupembha ujhe ni umsanjike manja, nayo siwakhale wamoyo.”
19Yesu wadachoka pamojhi ni oyaluzidwa wake, adachatana ni yujha wamkulu.
20Yapo amapita maye mmojhi uyo wamasusa nghole kwa vyaka khumi ni viwili, wadamchata Yesu mmbuyo, wadagafya njhonga ya njhalu ya Yesu. 21Wadaganizila mumtima mwake, “Nikagafyape njhalu yake, sinilame.”
22Yesu wadapenya mmbuyo wadamwona wamkazi yujha, wadamkambila, “Mwali, limba mtima! Chikulupi chako chakulamicha.” Pampajha wamkazi yujha wadalama.
23Ndiipo Yesu wadalowa uti mnyumba ya wamkulu yujha. Yapo wadaona wandhu yawo amaliza vitolilo va nyimbo za zaya, 24wadaakambila, “Chokani kubwalo! Mwaliyu siwadamwalile, nambho wangogonape.” Anyiiwo adamseka. 25Yapo adatuluchidwa kubwalo, Yesu wadalowa mnyumba, wadamgwila jhanja mwali yujha, nayo wadaima. 26Nghani imeneyo idaenela mujhiko lonjhe.
Yesu waalamicha osapenya awili
27Yesu yapo wamachoka pamalo pamenepo, yapo wadali mnjila, osapenya awili adamchata, adakamba, “Mwana wa Daudi, utilengele lisungu!”
28Yesu yapo wadalowa mnyumba, wajha osapenya awili adamchata, wadaafunjha, “Bwanji, mkhulupilila kuti nikhoza kukulamichani?”
Anyiiwo adamuyangha, “Yetu, Ambuye.”
29Yesu wadaagafya maso yao, wadakamba, “Ikhale chimwecho ngati umo mukhulupilila.” 30Maso yao yadakhoza kupenya. Yesu wadakaniza kupunda, “Msadamkambila mundhu waliyonjhe vindhu ivi!”
31Nambho anyiiwo adachoka, adaeneza nghani za Yesu mujhiko lonjhe lijha.
Yesu wamlamicha uyo siwakhoza kukamba
32Wandhu yapo amabwela kwao, wandhu wina adampelekela Yesu mundhu uyo simakhoze kukamba ndande wadali ni chiwanda. 33Pampajha chiwanda yapo chidachochedwa, mundhu yujha siwamakhoze kukamba wadayamba kukamba. Wandhu adadabwa ni kukamba, “Sichidaonekepo chindhu ngati ichi sichidachokelepo mujhiko la Izilaeli.”
34Nambho Afalisayo amakamba, “Wamkulu wa viwanda nde uyo wampacha Yesu mbhavu yotochocha viwanda.”
Yesu waalengela lisungu wandhu
35Yesu wamaendaenda mmijhi ni mvijhijhi, wamayaluza mnyumba zao zokomanilana Ayahudi ni wadaalalikila Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mnungu, ni kulamicha matenda ni mavuto yonjhe. 36Yesu yapo wadaona wandhu magulu kwa magulu, wadalengela lisungu ndande adali ni mandha ni adamwazika ngati mbelele zilibe owesa. 37Pamenepo wadaakambila oyaluzidwa wake, “Vokolola ni vambili, nambho wandhu wochita njhito ni wochepa. 38Mwaapembhe Ambuye Mnungu mwene vokolola apeleke ochita njhito mmunda mwake.”

Actualmente seleccionado:

Matayo 9: NTNYBL2025

Destacar

Compartir

Copiar

None

¿Quieres tener guardados todos tus destacados en todos tus dispositivos? Regístrate o inicia sesión