Matayo 10
10
Atumwi khumi ni awili
Maluko 3:13-19; Luka 6:12-16
1Yesu wadaatana wandhu wake wajha wayaluza khumi ni awili, wadaapacha ulamulilo wakuchocha viwanda ni kulamicha wodwala ni mavuto yonjhe. 2Maina ya atumwi khumi ni awili nde yaya, Simoni uyo watanidwanjho Petulo ni Anduleya uyo wadali mbale wake Petulo ni Yakobo mwana wa Zebedayo ni mbale wake uyo wadatanidwa Yohana, 3Filipo ni Batolomayo, Tomaso ni Matayo uyo wamalandila malipilo, ni Yakobo mwana wa Alufayo, ni Tadeyi, 4Simoni uyo wamabulanila jhiko lake, ni Yuda Isikalioti uyo wadamng'anamuka Yesu.
Yesu waatuma atumwi khumi ni awili
Maluko 6:7-13; Luka 9:1-6
5Yesu wadaatuma atumwi khumi ni awili wajha ni kwaalamula, “Msadapita kwa wandhu yawo samjhiwa Mnungu, kapina kulowa mmujhi wa Asamaliya. 6Nambho pitani kwa wandhu a jhiko la Izilaeli yawo ali ngati mbelele izo zasowa. 7Pitani mkalalikile wandhu Uthenga uwu, ‘Ufumu wa kumwamba wawandikila.’ 8Mwaalamiche odwala, ahyucheni akufa, alamicheni a makate, chochani viwanda. Anyiimwe mwapachidwa chajhe, chochani chajhe. 9Msatenga zahabu mmatumba yanu, kapina siliva, kapina gelenjha za shaba. 10Msadatenga thumba lakupembhela ndalama mnjila, kapina vivalo viwili, kapina malapasi, wala mpulu. Pakuti uyo wachita njhito wafunika wapachidwe mkokolo wake.”
11“Mkalowa mmujhi uliwonjhe kapina chijhijhi chalichonjhe, mfuneni mundhu uyo wakhoza kukulandilani, khalani mnyumba imeneyo mbaka pajha simchokepo. 12Yapo simulowe mnyumba, mwaalonjele wene khomo kwa kwambila mtendele ukhale namwe. 13Wene khomo akakulandilani bwino, anyiiwo siakhale kwa mtendele. Nambho ngati siakulandilani, anyiimwe simkhale kwa mtendele. 14Mundhu waliyonjhe wakakana kukulandilani kapina kukuvechelani, yapo simujhichoka, yakung'undheni malifumbi ya mmyendo mwanu kulangiza chizindikilo kuti akana kuulandila uthenga wa Mnungu. 15Zene nikukambilani, pa siku la lamulo Mnungu siwalange kupunda wandhu ngati achameneo kupitilila wandhu mijhi ya sodoma ni Gomola.”
Mavuto yayo yakujha
Maluko 13:9-13; Luka 21:12-17
16“Vechelani, ine nikutumani anyiimwe ngati mbelele pakati pa mibinji. Mkhale ochenjela ngati njoka, ni apole ngati nghunda. 17Mkhale maso ni wandhu sakuchucheni, chimwecho sakugwileni ni kukupelekani kunyumba ya milandu ni kukubulani mnyumba yokomanilana Ayahudi. 18Simupelekedwe kwa alamuli ni afumu ndande ya ine, dala mwaalalikile Uthenga Wabwino kwa anyiiwo ni kwa wandhu yao osati Ayahudi. 19Yapo sakupelekeni kubwalo la milandu, msadakhala ni mandha kuti simukambe chiyani, pakuti simupachidwe chokamba ndhawi imeneyo. 20Pakuti osati anyiimwe mukamba, nambho Mzimu Woyela wa Mnungu siukambe kupitila anyiimwe.”
21“Mbale siwamnga'namuke mbale wake kuti wphedwe, ni tate siwamung'anamuke mwana wake, wana nawo siwang'anamuke obala wao ni kwa wapha. 22Wandhu wonjhe siakuipileni ndande ya kunikhulupilila ine. Nambho yujha siwalimbe mtima mbaka pothela, ndeuyo siwalamichidwe. 23Wandhu akakuvutichani pamujhi thawilani mujhi wina. Zene nikukambilani, simumaliza njhito yanu mmijhi yonjhe ya Izilaeli popande Mwana wa Mundhu kujha.”
24“Palibe oyaluzidwa uyo wakhala wamkulu kupitilila oyaluza wake, kapina kapolo uyo wakhoza kukhala wamkulu kumpitilila mbuye wake. 25Mundhu wayaluzidwa wafunika wakhale ngati oyaluza wake, ni kapolo wakhale ngati ambuye wake. Ngati wamkulu wa nyumba amamtana Belizebuli, bwanji, wandhu amnyumba mwake siatanidwa mayina yoipa kupunda?”
Yani wa kumuopa
Luka 12:2-7
26“Chimwecho, msadaaopa wandhu. Abisa vindhu achichita, nambho kuli ndhawi ikujha wandhu saone ivo avibisa ni kila mundhu siwajhiwe visisi vao. 27Yajha nakukambilani yapo tidali tekha, anyiimwe mkambileni kila mundhu, ni yajha nakukambilani konong'ona anyiimwe mkambileni kila mundhu. 28Msadaopa yawo akhoza kukuphani anyiimwe, nambho sakhoza kuyomwecha mizimu yanu. Nambho muopeni yujha wakhoza kuyomwecha thupi pamojhi ni mzimu mumoto wa muyaya. 29Bwanji, njhete ziwili zigulichidwa kwa senti imojhi? Nambho palibe ata imojhi iyo ikufa popande Atate wanu akumwamba kujhiwa. 30Nambho anyiimwe, ata chichi la mmitu yanu lawelengedwa lonjhe. 31Chimwecho msadaopa, anyiimwe amate kupunda kupitilila mbalame!”
Kumvomela ni kumkana Yesu
Luka 12:8,9
32“Mundhu waliyonjhe uyo siwavomele pachogolo pa wandhu kuti iye ni wanga, ine nane sinimvomele pamaso pa Atate wanga yawo ali ku mwamba. 33Nambho mundhu waliyonjhe uyo siwanikane pachogolo pa wandhu, ine nane sinimkane pamaso pa Atate wanga aku mwamba.”
Sinidapeleke mtendele nambho upanga
Luka 12:51-53; 14:26,27
34“Msadaganiza kuti najha kwaachita wandhu akhale kwa mtendele pajhiko. Notho. Sinidajhe kwaachita wandhu akhale kwa mtendele, nambho najha kupeleka upanga. 35Pakuti najha kwaachita ayambane mnyamata ni atate wake, mwali ni maye wake, mpongozi wamkazi ni mpongozi wake, 36ni adani a mundhu ni wandhu wajha ali mnyumba mwake.”
37“Mundhu waliyonjhe uyo waakonda atate wake kapina amaye wake kupitilila ine, mmeneyo siwakhoza kukhala oyaluzidwa wanga. Ni mundhu waliyonjhe waakonda anamwali wake kapina wana wake waachimuna kupitilila ine, mmeneyo siwakhoza kukhala oyaluzidwa wanga. 38Mundhu uyo siwavomela kuvutika ni kunichata ine, mmeneyo siwakhoza kukhala oyaluzidwa wanga. 39Mundhu waliyonjhe uyo siwaulonde umoyo wake siwausoweze, nambho waliyonjhe uyo wausoweza umoyo wake ndande ya ine, siwaupate umoyo wa muyaya.”
Chikho
Maluko 9:41
40“Mundhu waliyonjhe uyo wakulandilani anyiimwe kukhomo lake, wanilandila ine ni mundhu uyo wanilandila ine, wamlandila yujha wanituma. 41Mundhu waliyonjhe uyo wamulandila mlosi ndande ni mlosi, siwalandile chikho cha ulosi. Mundhu waliyonjhe uyo wamlandila mundhu wabwino ndande ni mundhu wabwino, siwalandile chikho cha kukhala mundhu wabwino. 42Nikukambilani uzene, mundhu waliyonjhe uyo siwampache mmojhi wa oyaluzidwa yawa chikho cha majhi yozizila ndande yakukhala oyaluzidwa wanga, zenedi siwapate chikho chake.”
Actualmente seleccionado:
Matayo 10: NTNYBL2025
Destacar
Compartir
Copiar

¿Quieres tener guardados todos tus destacados en todos tus dispositivos? Regístrate o inicia sesión
The New Testament in Nyanja @The Word for The World International and Nyanja Language translation, 2025. All rights reserved.

: